Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.
2 Akorinto 4:12 - Buku Lopatulika Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero ife timaperekedwa ku imfa, koma chimenechi chimakupatsani moyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu. |
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.
Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
Pakuti tikondwera, pamene ife tifooka ndi inu muli amphamvu; ichinso tipempherera, ndicho ungwiro wanu.
Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa.
Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula;
Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.
Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.