Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.
2 Akorinto 10:9 - Buku Lopatulika kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa makalatawo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa akalatawo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono musayese kuti ndikungokuwopsezani ndi makalata anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine sindikufuna kuoneka ngati ndikukuopsezani ndi makalata anga. |
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.
Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.
Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;