Taonani, ndi machira a Solomoni; pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi, a mwa ngwazi za Israele.
1 Samueli 8:16 - Buku Lopatulika Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Idzakulandani antchito anu aamuna ndi adzakazi anu. Idzakulandaninso ng'ombe zanu zonenepa ndi abulu anu, ndi kumazigwiritsa ntchito zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumuyo idzatenga antchito anu aamuna ndi aakazi. Idzatenganso ngʼombe zanu zabwino ndi abulu anu nʼkumazingwiritsa ntchito. |
Taonani, ndi machira a Solomoni; pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi, a mwa ngwazi za Israele.
Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;
Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yampesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake.