Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.
1 Samueli 7:11 - Buku Lopatulika Ndipo Aisraele anatuluka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betekara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aisraele anatuluka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betekara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aisraele adatuluka ku Mizipa naŵalondola Afilistiwo, mpaka kubzola Betekara, akuŵapha njira yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli anatuluka ku Mizipa kuthamangitsa Afilisti aja nʼkumawapha mʼnjira yonse mpaka kumunsi kwa Beti-Kari. |
Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.
Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.
Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.