1 Samueli 3:8 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adamuitananso Samuele kachitatu. Pompo adadzukanso, napita kwa Eli, nakanena kuti, “Ndabwera, mwandiitana ndithu basi.” Pamenepo Eli adazindikira kuti Chauta ndiye amene ankaitana mnyamatayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anayitananso Samueli kachitatu ndipo Samueli anadzuka ndikupita kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera popeza mwandiyitana ndithu.” Apo Eli anazindikira kuti Yehova ndiye ankayitana mnyamatayo. |
Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m'malo mwake.