Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara.
1 Samueli 2:31 - Buku Lopatulika Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithudi, masiku akudza pamene ndidzachotse anyamata onse a m'banja la atate ako, kotero kuti siidzapezekanso nkhalamba pabanja pako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ikubwera imene ndidzachotsa anyamata ako ndi anyamata a pa banja la abambo ako, kotero kuti sipadzakhala munthu wokalamba pa banja lako. |
Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara.
Koma Aleviwo anandichokera kunka kutaliwo, posokera Israele, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.
Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.
Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.