Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.
1 Samueli 14:8 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziwulula kwa iwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziwulula kwa iwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yonatani adati, “Tiwolokere kwa anthuwo, ndipo tikadziwonetse kwa iwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anati, “Tiye tsono tiwoloke kupita kumene kuli anthuwo ndi kukadzionetsa kwa iwo. |
Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.
Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo.