Nateronso m'mizinda ya Manase, ndi Efuremu, ndi Simeoni, mpaka Nafutali, m'mabwinja mwao mozungulira.
1 Samueli 13:20 - Buku Lopatulika koma Aisraele onse ankatsikira kwa Afilisti, kuti awasanjire munthu yense chikhasu chake, cholimira chake, nkhwangwa yake, ndi chisenga chake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma Aisraele onse ankatsikira kwa Afilisti, kuti awasanjire munthu yense chikhasu chake, cholimira chake, nkhwangwa yake, ndi chisenga chake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Mwisraele aliyense ankapita kwa Afilisti kukasanjitsa pulao kapena khasu lake, ndi kukanoletsa nkhwangwa yake kapena chikwakwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Aisraeli onse amapita kwa Afilisti kukanoletsa mapulawo, makasu, nkhwangwa ndi zikwakwa zawo. |
Nateronso m'mizinda ya Manase, ndi Efuremu, ndi Simeoni, mpaka Nafutali, m'mabwinja mwao mozungulira.
ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida.
Ndipo m'dziko lonse la Israele simunapezeke wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisraele angadzisulire malupanga kapena mikondo;
ndipo mtengo wakukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mano unali masekeli awiri mwa atatu ndi mtengo wa nkhwangwazo; ndi kusongola zotwikira unali sekeli imodzi mwa atatu.