Ndipo akulu onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveke mlandu.
1 Samueli 10:15 - Buku Lopatulika Ndipo mbale wa atate wa Saulo anati, Undiuze chimene Samuele analankhula nawe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbale wa atate wa Saulo anati, Undiuze chimene Samuele analankhula nawe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mbale wa bambo wakeyo adati, “Ndikukupempha, uzeko zimene adanena Samuele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.” |
Ndipo akulu onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveke mlandu.
Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeze, tinadza kwa Samuele.
Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo.