Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.
1 Akorinto 3:4 - Buku Lopatulika Pakuti pamene wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mnzake, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti pamene wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mnzake, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumangoti ali apa, “Ine ndine wa Paulo,” ali apa, “Ine ndine wa Apolo.” Kodi mukamatero simukuchita ngati anthu odalira zapansipano? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene wina anena kuti, “Ine ndimatsatira Paulo,” ndipo wina akuti, “Ine ndimatsatira Apolo,” Kodi si inu akunja? |
Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.
pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?
Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.
Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.