Yuda 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Okondedwa, ngakhale ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso cha tonsefe, ndakakamizidwa kuti ndikulembereni ndi kukupemphani kolimba kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro chimene Mulungu anachipereka kamodzi kokha kwa anthu onse oyera mtima. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Inu okondedwa, ndinkafunitsitsa kukulemberani kalata, kuti ndikufotokozereni za chipulumutso chokhudza tonsefe. Ndiye mtima wanga udandikakamiza kuti ndikulembereni tsopano ndi kukupemphani kolimba, kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro, chimene Mulungu adapatsa anthu ake kamodzi kokhako. Onani mutuwo |
Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino