Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yuda 1:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndine Yuda, mtumiki wa Yesu Khristu, komanso mʼbale wake wa Yakobo. Kwa inu amene Mulungu Atate anakuyitanani, amene amakukondani ndikukusungani mwa Yesu Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndine, Yuda, mtumiki wa Yesu Khristu, ndiponso mbale wa Yakobe. Ndikulemba kalatayi kwa inu amene Mulungu adakuitanani, amene Mulungu Atate athu amakukondani ndi kukusungani, kusungira Yesu Khristu.

Onani mutuwo Koperani




Yuda 1:1
40 Mawu Ofanana  

Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo;


Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi?


Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote,


Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.


Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikarioti amene anamupereka.


Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.


Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?”


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.


Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo.


Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi.


Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni.


Ndipo chifuniro cha Iye amene anandituma Ine nʼchakuti ndisatayepo ngakhale ndi mmodzi yemwe mwa onse amene Iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza.


Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo.


“Tsopano ine ndikukuperekani kwa Mulungu ndiponso kwa mawu a chisomo chake, amene ali ndi mphamvu zokulitsa inu ndi kukupatsani chuma pakati pa onse amene anayeretsedwa.


Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine,


Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu


Inunso muli mʼgulu la Amitundu oyitanidwawo kukhala ake a Yesu Khristu.


Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa.


Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.


Iwo amene anawasankhiratu, anawayitananso. Amene Iye anawayitana anawalungamitsanso ndipo amene anawalungamitsa anawapatsanso ulemerero.


ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina.


Kupita ku mpingo wa Mulungu ku Korinto, kwa oyeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi oyitanidwa kukhala opatulika ndiponso kwa onse amene amapemphera mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu mʼdziko lonse lapansi, amene ndi Ambuye wawo ndi wathunso.


Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.


kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake.


kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.


Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu.


Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe.


Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya.


Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.


Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana. Landirani moni.


Mulungu Atate anakusankhani, atakudziwani kuyambira pachiyambi, ndipo Mzimu Woyera wakuyeretsani kuti mumvere Yesu Khristu ndikutsukidwa ndi magazi ake. Chisomo ndi mtendere zikhale ndi inu mochuluka.


Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza.


Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.


Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba.


Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.


Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha.


Okondedwa, ngakhale ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso cha tonsefe, ndakakamizidwa kuti ndikulembereni ndi kukupemphani kolimba kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro chimene Mulungu anachipereka kamodzi kokha kwa anthu onse oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa