Obadiya 1:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wako pa nthawi ya tsoka lake, kapena kunyogodola Ayuda chifukwa cha chiwonongeko chawo, kapena kuwaseka pa nthawi ya mavuto awo. Onani mutuwoBuku Lopatulika12 Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Inu simukadayenera kuŵanyodola abale anu Ayuda chifukwa cha tsoka lao. Simukadayenera kukondwerera kuwonongeka kwao. Simukadayenera kuŵaseka pamene iwo anali m'mavuto. Onani mutuwo |
Kudzera mwa amithenga ako iwe wanyoza Ambuye. Ndipo wanena kuti, ‘Ndi magaleta anga ochuluka ndafika pamwamba pa mapiri, pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni. Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri, ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini. Ndafika pa msonga pake penipeni, nkhalango yake yowirira kwambiri.