Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Obadiya 1:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pamene adani ankamulanda chuma chake pamene alendo analowa pa zipata zake ndi kuchita maere pa Yerusalemu, pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ake, nalowa m'zipata zake achilendo, nachitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ake, nalowa m'zipata zake achilendo, nachitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Munkangoonerera pamene adani ankaŵalanda chuma chao, munkachita ngati kuvomerezana nawo, amene ankaloŵa pa zipata za Yerusalemu, namagaŵana chumacho.

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:11
13 Mawu Ofanana  

Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.


Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita pa tsiku limene Yerusalemu anagonja. Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi mpaka pa maziko ake!”


Ukaona wakuba umamutsatira, umachita maere ako pamodzi ndi achigololo


Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:


Matenti a Edomu ndi Aismaeli, Mowabu ndi Ahagiri,


“Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo.


Anagawana anthu anga pochita maere ndipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere; anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyo kuti iwo amwe.


Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthu ndi kuwugulitsa ku Edomu,


Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu, osasunga pangano laubale lija,


Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa ndipo anapita ku ukapolo. Ana ake anawaphwanyitsa pansi mʼmisewu yonse ya mu mzindamo. Anachita maere ogawana anthu ake otchuka, ndipo anthu ake onse amphamvu anamangidwa ndi maunyolo.


Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo, chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa