Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 9:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mose anawayankha kuti, “Dikirani mpaka nditamva zimene Yehova walamula zokhudza Inu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve chouza Yehova za inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve chouza Yehova za inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mose adayankha kuti, “Dikirani kuti ndimve zimene Chauta alamule za inu.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:8
19 Mawu Ofanana  

Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”


Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa; amawulula pangano lake kwa iwowo.


Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.


Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso.


Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna.


Ukawawuze ndithu mawu anga, kaya akamva kaya sakamva. Paja anthuwa ndi awupandu.


“Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza.


Anamuyika mʼndende mpaka atadziwa bwino chofuna cha Yehova.


ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye.


Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova


ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?”


Ndipo Yehova anawuza Mose kuti,


Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine.


Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha.


Pakuti sindinakubisireni pokulalikirani chifuniro chonse cha Mulungu.


Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi.


Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, koma sikuti ndine wolungama. Wondiweruza ine ndi Ambuye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa