Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 9:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Zinkachitika motere mosalekeza: mtambo unkakhala pamwamba pa chihema, ndipo usiku unkaoneka ngati moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Kudatero kosalekeza; mtambo umachiphimba, ndi moto umaoneka usiku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Kudatero kosalekeza; mtambo umachiphimba, ndi moto umaoneka usiku.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Zinkachitika motero mosalekeza. Mtambowo unkaphimba chihema chamsonkhano masana, ndipo usiku unkaoneka ngati moto.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:16
13 Mawu Ofanana  

Masana munkawunikira ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawunikira ndi chipilala cha moto njira yonse imene ankayendamo.


“Koma Inu ndi chifundo chanu chachikulu, simunawasiye mʼchipululu. Chipilala cha mtambo sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo masana ndipo chipilala cha moto sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo usiku.


Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo, ndi moto owawunikira usiku.


Anawatsogolera ndi mtambo masana ndi kuwala kwa moto usiku wonse.


Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.


Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.


Pakuti sindikufuna kuti inu mukhale osadziwa zenizeni, abale, kuti makolo athu anatsogozedwa ndi mtambo ndikuti onse anawoloka nyanja.


Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso.


amene anakutsogolerani pa ulendo wanu, ndi moto nthawi ya usiku ndi mtambo nthawi ya masana, kukufunirani malo woti mumange msasa ndi kukuonetsani njira yoti muyendemo.


Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa