Numeri 7:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; Onani mutuwoBuku Lopatulika14 chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani. Onani mutuwo |
Atamaliza, iwo anabweretsa ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, ndipo anazigwiritsira ntchito popangira zida za mʼNyumba ya Yehova: ziwiya zogwiritsa ntchito potumikira ndi popereka nsembe zopsereza, komanso mbale ndi ziwiya zagolide ndi siliva. Nthawi yonse ya moyo wa Yehoyada, nsembe zopsereza zinkaperekedwa mosalekeza mʼNyumba ya Yehova.