Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 7:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, ndi beseni lasiliva limodzi lowazira, lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo wopatulika ndipo zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka chachakudya;

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

13 chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:13
23 Mawu Ofanana  

maphaka khumi pamodzi ndi mabeseni khumi pa maphakawo;


miphika, mafosholo ndi mbale zowazira magazi. Ziwiya zonsezi za ku Nyumba ya Yehova, zimene Hiramu anapangira Mfumu Solomoni, zinali zamkuwa wonyezimira.


ndipo ndinawayezera siliva ndi golide, ndiponso ziwiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi alangizi ake, nduna zake ndi Aisraeli onse amene anali kumeneko anazipereka.


Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe.


Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova.


Ndipo anapanga ziwiya za pa tebulolo zagolide wabwino, mbale ndi zipande, mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe za chakumwa.


Nebuzaradani uja anatenganso mabeseni, ziwiya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoyikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho ndi zina zonse zagolide ndi siliva.


Pamene Belisazara ankamwa vinyo, analamula kuti ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara abambo ake anakatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu zikatengedwe kuti mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi amweremo.


“ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani,


Potchula mtengo uliwonse wansembe awerengere molingana ndi mtengo wa sekeli wa ku Nyumba ya Mulungu: magera makumi awiri pa sekeli imodzi.


mtengo wake ukhale masekeli a siliva makumi asanu, molingana ndi kawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu, ngati munthuyo ndi wamwamuna wa zaka zapakati pa 20 ndi 60.


Pa tsiku limenelo pa maberu a akavalo padzalembedwa mawu oti wopatulikira Yehova, ndipo miphika ya mʼNyumba ya Yehova idzakhala yopatulika ngati mbale za ku guwa.


munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi.


Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi.


Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma.


utenge masekeli asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale ofanana ndi masekeli a ku malo wopatulika, kumene sekeli imodzi imakwanira magera makumi awiri.


Amene anabweretsa chopereka chake tsiku loyamba anali Naasoni mwana wa Aminadabu wa fuko la Yuda.


mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;


Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;


Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake.


Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa