Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 5:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma munthu akapanda kukhala ndi wachibale woti nkulandira zinthu zobwezedwa zija m'malo mwa zoonongedwazo, apereke zobwezedwazo kwa Chauta kuti zikhale za wansembe, kuwonjezera pa nkhosa yamphongo yadipo ija imene amachitira mwambo wopepesera machimo ake.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:8
8 Mawu Ofanana  

Ndalama zomwe zinkaperekedwa pa nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo sanabwere nazo ku Nyumba ya Yehova pakuti zinali za ansembe.


Munthuyo ayenera kubweza zinthu zopatulika zimene sanaperekezo. Awonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse ndi kuzipereka zonsezo kwa wansembe amene adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nkhosa yayimuna ija ngati nsembe yopepesera ndipo wochimwayo adzakhululukidwa.


kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse.


“ ‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake.


ayenera kuwulula tchimo limene anachitalo. Ayenera kubweza zonse zimene anawononga, ndipo awonjezerepo chimodzi mwa magawo asanu ndi kuzipereka kwa munthu amene anamulakwirayo.


Zopereka zonse zopatulika zomwe Aisraeli abwera nazo kwa wansembe zikhale za wansembeyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa