Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 5:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 ayenera kuwulula tchimo limene anachitalo. Ayenera kubweza zonse zimene anawononga, ndipo awonjezerepo chimodzi mwa magawo asanu ndi kuzipereka kwa munthu amene anamulakwirayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 azivomereza tchimo lake adalichita; nabwezere chopalamulacho monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kuchipereka kwa iye adampalamulayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 azivomereza tchimo lake adalichita; nabwezere chopalamulacho monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kuchipereka kwa iye adampalamulayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Aulule tchimo limene wachimwalo. Abweze zonse zimene adaononga, ndipo aonjeze chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake ndi kupatsa amene adamchimwirayo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:7
14 Mawu Ofanana  

Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” Sela


Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.


“ ‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane,


zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo,


“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa mosadziwa posapereka zinthu zopatulika zofunika kwa Yehova, munthuyo apereke kwa Yehova nsembe yopepesera machimo ake. Nsembeyo ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale wokwana masekeli oyenera a siliva pakawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula.


Munthuyo ayenera kubweza zinthu zopatulika zimene sanaperekezo. Awonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse ndi kuzipereka zonsezo kwa wansembe amene adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nkhosa yayimuna ija ngati nsembe yopepesera ndipo wochimwayo adzakhululukidwa.


“ ‘Pamene munthu wazindikira kuti wachimwa motere, awulule tchimo limene wachitalo.


“ ‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake.


Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake.


Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”


Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa