Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 4:25 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

25 azinyamula nsalu zophimba za Kachisi, ndi chihema chokomanako, chophimba chake, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu chili pamwamba pake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 azinyamula nsalu zophimba za Kachisi, ndi chihema chokomanako, chophimba chake, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu chili pamwamba pake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 azinyamula nsalu zochinga malo opatulika, chihema chamsonkhano pamodzi ndi chophimbira chake, zikopa zambuzi zophimba pamwamba pake, ndiponso nsalu zochinga pa khomo la chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:25
8 Mawu Ofanana  

“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.


Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.


Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose.


Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.


“Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi:


Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa