Numeri 4:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 “Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake. Onani mutuwoBuku Lopatulika12 Natenge zipangizo zake zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsalu yamadzi, ndi kuziphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pachonyamulira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Natenge zipangizo zake zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsalu yamadzi, ndi kuziphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pachonyamulira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Atenge zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito m'malo opatulika, aziike m'nsalu yobiriŵira, ndipo aziphimbe ndi zikopa zambuzi, ndi kuziika pa chonyamulira chake. Onani mutuwo |