Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 4:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo achimange ndi chipangizo zake zonse m'chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa chonyamulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo achimange ndi chipangizo zake zonse m'chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa chonyamulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndipo achiike pamodzi ndi zipangizo zake zonse m'thumba la zikopa zambuzi, ndi kuchiika pa chonyamulira chake.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:10
6 Mawu Ofanana  

“Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi.


zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha;


“Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira.


“Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake.


Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.


“Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa