Numeri 32:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo. Onani mutuwoBuku Lopatulika1 Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali ndi ng'ombe zambiri. Adaona dziko la Yazere ndi dziko la Giliyadi kuti linali ndi malo oyenera kuŵeterako ng'ombe. Onani mutuwo |
Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo.