Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 3:25 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ntchito imene Ageresoni anapatsidwa ku tenti ya msonkhano inali yosamalira Chihema ndi tenti, pamodzi ndi zophimbira zake, katani ya pa khomo la ku tenti ya msonkhano,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

25 Ndipo udikiro wa ana a Geresoni m'chihema, chokomanako ndiwo Kachisi, ndi chihema, chophimba chake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo udikiro wa ana a Geresoni m'chihema, chokomanako ndiwo Kachisi, ndi chihema, chophimba chake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Ndipo ntchito imene ana a Geresoni adapatsidwa m'chihema chamsonkhano inali yosamala chihema cha Mulungu, pamodzi ndi chophimbira chake, nsalu yochinga pakhomo pa chihema chamsonkhano,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:25
23 Mawu Ofanana  

Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.


Hezekiya anakhazikitsa magulu a ansembe ndi Alevi, gulu lililonse monga mwa ntchito zawo ngati ansembe kapena Alevi, kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kutumikira, kuyamikira ndi kuyimba matamando pa zipata za ku malo okhala Yehova.


Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere.


Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose.


Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema.


Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.


Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka.


Mtsogoleri wa mabanja a Ageresoni anali Eliyasafu mwana wa Laeli.


Azigwira ntchito yothandiza iyeyo ndi gulu lonse ku tenti ya msonkhano pogwira ntchito ya ku Chihema.


Anapereka ngolo ziwiri ndi ngʼombe zothena zinayi kwa Ageresoni monga mwantchito yawo


Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.


Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”


Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa