Numeri 28:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Awuze kuti, ‘Nsembe ya chakudya imene muzipereka pa moto kwa Yehova tsiku ndi tsiku ndi iyi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri, wopanda chilema. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Ndipo uŵauzenso kuti, nsembe yotentha pa moto, yoti muzipereka kwa Chauta ndi iyi: Muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, kuti akhale nsembe yosalekeza. Onani mutuwo |
Kenaka ndinamva wina akuyankhula; ndipo woyera winanso anamufunsa kuti, “Kodi zimene ndikuziona mʼmasomphenyazi zidzatha liti? Nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku zidzakhala zoletsedwa mpaka liti? Nanga chonyansa chosokoneza chidzakhalapo mpaka liti? Kodi gulu la ankhondo lidzapondereza malo opatulika mpaka liti?”