Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 27:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ana aakazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ana akazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Ana aakazi a Zelofehadiwo akunena zoona. Uŵapatse choloŵa chao pakati pa abale a bambo wao. Uŵapatse choloŵa cha bambo waocho kuti chikhale chao.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 27:7
10 Mawu Ofanana  

Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo.


Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.


‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza. Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”


ndipo Yehova anati kwa iye,


“Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi.


Tsono mwa lamulo la Yehova, Mose anapereka lamulo ili kwa Aisraeli: “Zimene ana a Yosefe akunena ndi zoona.


Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo


Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.


Iwo anapita kwa Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri ndipo anati: “Yehova analamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse cholowa chathu.” Choncho iwowo pamodzi ndi abale a abambo awo anawapatsa dera lina la dzikolo kuti likhale monga mwa lamulo la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa