Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 27:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Kenaka ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wamwamuna wa Manase, a mʼmabanja a Manase, mwana wa Yosefe anabwera. Mayina a ana aakaziwo anali awa: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anakayima

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Pamenepo anayandikiza ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo anayandikiza ana akazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nthaŵi imeneyo kudabwera ana aakazi a Zelofehadi. Iyeyo anali mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, a m'mabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana ake aakaziwo anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 27:1
6 Mawu Ofanana  

Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka. Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha.


(Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)


pa chipata cha tenti ya msonkhano pamaso pa Mose, wansembe Eliezara, atsogoleri ndi anthu onse, ndipo anati,


Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa