Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 26:53 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

53 “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

53 Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

53 Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

53 “Uŵagaŵire dziko anthu ameneŵa, kuti likhale choloŵa chao, molingana ndi chiŵerengero cha maina ao.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:53
16 Mawu Ofanana  

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.


Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.


“Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani monga cholowa chimene udzachilandira.”


Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,


Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda, ndipo imfa idzawadya. Olungama adzawalamulira mmawa; matupi awo adzavunda mʼmanda, kutali ndi nyumba zawo zaufumu.


Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli.


Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ”


Yehova anawuza Mose kuti,


Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa.


Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.


Odala ndi amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.


“Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima, chifukwa iwe udzatsogolera anthu awa kukalandira dziko limene Ine ndinalonjeza makolo awo kuti ndidzawapatsa.


Choncho Yoswa anagonjetsa dziko lonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Tsono Yoswa analipereka kwa Aisraeli kuti likhale lawo, fuko lililonse gawo lake. Anthu onse anapumula, osamenyanso nkhondo.


Umu ndi mmene Aisraeli analandirira cholowa chawo mʼdziko la Kanaani. Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni pamodzi ndi akuluakulu a mafuko a Israeli ndiwo anagawa dzikolo kugawira Aisraeli.


Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.


Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu, ndipo adzalamulira dziko lapansi.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa