Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 26:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi: kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki; kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana aamuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Fuko la Rubeni. Rubeni anali mwana wachisamba wa Israele. Ana aamuna a Rubeni anali aŵa: Hanoki anali kholo la banja la Ahanoki. Palu anali kholo la banja la Apalu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:5
11 Mawu Ofanana  

Leya anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha Rubeni pakuti anati, “Yehova waona kusauka kwanga. Zoonadi, mwamuna wanga adzandikonda tsopano.”


Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi. Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri:


Ana a Leya ndi awa: Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni.


Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa,


ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi.


Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni.


Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.


“Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:


kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa