Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 24:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Apo Balaki adapsera mtima Balamu, ndipo adaomba m'manja. Tsono Balakiyo adauza Balamu kuti, “Paja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, ndipo inu mwaŵadalitsa katatu konseka.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:10
15 Mawu Ofanana  

Paja iwowa sanawachingamire Aisraeli kukawapatsa chakudya ndi madzi. Mʼmalo mwake analemba ganyu Baalamu kuti adzawatemberere. Komabe Mulungu wathu anasandutsa tembererolo kukhala mdalitso.


Mphepoyo imamuwomba ndithu ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”


“Tsono mwana wa munthu, nenera ndipo uwombe mʼmanja. Lupanga likanthe kawiri ngakhale katatu. Limenelo ndilo lupanga lophera anthu. Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa limene likuwazungulira.


Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga, ndipo ndidzaziziritsa ukali wanga Ine Yehova ndayankhula.”


“ ‘Koma Ine ndachita kuwomba mʼmanja kuti phuu nʼkudabwa chifukwa cha phindu lachinyengo limene mwapeza ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika pakati panu.


‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’ ”


chifukwa ndidzakulipira bwino kwambiri ndipo ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene. Bwera ndipo uwatemberere anthu amenewa mʼmalo mwanga.’ ”


Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.”


Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!”


Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”


Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi, monga mkango waukazi, adzamuputa ndani? “Amene adalitsa iwe, adalitsike ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”


Zimenezi zinachitika katatu ndipo kenaka zonse zinatengedwa kupita kumwamba.


Musachite nawo mgwirizano uliwonse wa mtendere pa moyo wanu wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa