Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 24:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zina zija, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yake kuchipululu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yake kuchipululu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pamene Balamu adaona kuti zinali zokondwetsa Chauta kuti adalitse Aisraele, sadapite monga nthaŵi zina zija kukafunsa kuti adziŵe zimene Mulungu akufuna, koma adangotembenuka nayang'ana ku chipululu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:1
13 Mawu Ofanana  

Mmawa mwake Balaamu anadzuka ndi kuwuza akuluakulu a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko la kwanu chifukwa Yehova sanandilole kuti ndipite nanu.”


Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena.


Balaamu anawuza Balaki kuti, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu pamene ine ndikukakumana ndi Mulungu cha uko.”


Wandilamula kuti ndidalitse, Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe.


Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo, palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli. Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti, ‘Onani zimene Mulungu wachita!’


Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu.


Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu.


Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse.


Paja iwo ndi amene ankatsatira uphungu wa Balaamu ndiponso ndi amene anachititsa Aisraeli kuti asiye Yehova pa zimene zinachitika ku Peori, kotero mliri unagwera anthu a Yehova.


Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo.


Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako.


Choncho Sauli ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake 3,000 napita ku chipululu cha Zifi kukafunafuna Davide ku chipululuko.


Ndipo Sauli anawuza Davide kuti, “Yehova akudalitse iwe Davide mwana wanga. Udzachita zinthu zazikulu ndipo udzapambana.” Choncho Davide anayenda njira yake ndipo Sauli anabwerera kwawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa