Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 23:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kuchokera pamwamba pa mapiri ndikuona anthu, ndikuwaona kuchokera pa zitunda. Ndikuona anthu okhala pawokha, osakhala mʼgulu limodzi ndi mitundu ina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Pakuti, pokhala pamwamba pa matanthwe ndimpenya, pokhala pa zitunda ndimuyang'ana; taonani, ndiwo anthu akukhala pa okha. Osadziwerengera pakati pa amitundu ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti, pokhala pamwamba pa matanthwe ndimpenya, pokhala pa zitunda ndimuyang'ana; taonani, ndiwo anthu akukhala pa okha. Osadziwerengera pakati pa amitundu ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Pamene ndikuŵaona kuchokera pamwamba pa phiri, pamene ndikuŵayang'ana kuchokera ku mapiri, ndikuwona anthu okhala paokha, osadziŵerengera kumodzi ndi mitundu ina.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:9
15 Mawu Ofanana  

Zomwe zikuchitika ndi izi. Aisraeli ena ndi ana awo aamuna anayamba kukwatira ana aakazi a anthuwa. Choncho mtundu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a mʼderali. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo akupambana pa makhalidwe osakhulupirikawa.”


Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere.


Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?”


Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe,” akutero Yehova. “Ndidzawonongeratu mitundu yonse ya anthu a ku mayiko kumene ndakupirikitsira, Koma iwe sindidzakuwononga kotheratu. Ndidzakulanga iwe ndithu koma moyenerera; sindidzakulekerera osakulanga.”


“Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere, umene ukukhala mosatekeseka,” akutero Yehova, “mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo; anthu ake amakhala pa okha.


“Pakuti ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amasefera ufa mʼsefa, koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.


Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza, nkhosa zimene ndi cholowa chanu, zimene zili zokha mʼnkhalango, mʼdziko la chonde. Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi monga masiku akale.


Nʼchifukwa chake “Tulukani pakati pawo ndi kudzipatula, akutero Ambuye. Musakhudze chodetsedwa chilichonse, ndipo ndidzakulandirani.”


Pamene Wammwambamwamba anapereka mayiko kwa anthu a mitundu ina kukhala cholowa chawo, pamene analekanitsa anthu onse, anayikira malire anthu onse molingana ndi chiwerengero cha ana a Israeli.


Motero Israeli adzakhala yekha mwamtendere; zidzukulu za Yakobo zili pa mtendere mʼdziko la tirigu ndi vinyo watsopano, kumene thambo limagwetsa mame.


amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.


Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa