Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 23:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndingatemberere bwanji amene Mulungu sanawatemberere? Ndinganyoze bwanji amene Yehova sanawanyoze?

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberere? Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoze?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberere? Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoze?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma ine ndingathe bwanji kumtemberera amene Mulungu sadamtemberere? Ndingathe bwanji kumufunira zoipa amene Chauta sadamfunire zoipa?

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:8
8 Mawu Ofanana  

Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira, ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.


Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga, ndipo ndimapusitsa owombeza mawula. Ndimasokoneza anthu a nzeru, ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.


Koma Mulungu anawuza Balaamu kuti, “Usapite nawo. Usawatemberere anthu amenewo chifukwa ndi odalitsika.”


Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.”


Wandilamula kuti ndidalitse, Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe.


Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo, palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli. Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti, ‘Onani zimene Mulungu wachita!’


Ndipo Balaamu ananena uthenga wake: “Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu, mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa. Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga, pita nyoza Israeli.’


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa