Numeri 21:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa ndi kuyipachika pa mtengo. Ndipo aliyense wolumidwa akayangʼana njoka yamkuwayo ankakhala ndi moyo. Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Choncho Mose adapanga njoka yamkuŵa, naipachika pa mtengo. Ndiye ankati wina aliyense njoka ikamuluma, munthuyo akayang'ana njoka yamkuŵa ija, ankakhala moyo. Onani mutuwo |
“Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa.