Numeri 21:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Aisraeli anayenda kuchokera ku phiri la Hori kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira kuzungulira dziko la Edomu. Koma anthu anataya mtima mʼnjiramo Onani mutuwoBuku Lopatulika4 Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Aisraele adanyamuka ku phiri la Horo nadzera njira ya ku Nyanja Yofiira, kuzungulira dziko la Edomu. Koma pa njira adayamba kunyong'onyeka. Onani mutuwo |
“Pambuyo pake, Aisraeli ananyamuka ulendo kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo anafika ku mmawa kwa dziko la Mowabu ndi kumanga zinthando zawo ku mbali ina ya mtsinje wa Arinoni. Iwo sanalowe mʼdziko la Mowabu, chifukwa mtsinje wa Arinoni ndiwo unali malire a dziko la Mowabu.