Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 21:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yehova anamva pempho la Aisraeli ndipo anapereka Akanaaniwo kwa iwo. Anawawononga pamodzi ndi mizinda yawo. Kotero malowo anatchedwa Horima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi mizinda yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi midzi yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chauta adamvera mau a Aisraelewo naŵaperekadi Akanani aja m'manja mwao. Aisraele adaŵaonongeratu Akananiwo pamodzi ndi mizinda yao yomwe. Choncho malowo adaŵatcha kuti Horoma.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:3
11 Mawu Ofanana  

Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa; mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo.


Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo.


Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga; Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.


Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha; ndidzakhala naye pa mavuto, ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.


Koma Aamaleki ndi Akanaani amene ankakhala ku dziko lamapirilo anatsika ndi kumenyana nawo ndipo anawakantha mʼnjira yonse mpaka ku Horima.


Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima.


Komabe mʼmizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, musasiyemo chamoyo chilichonse.


mfumu ya Horima imodzi mfumu ya Aradi imodzi


Elitoladi, Kesili, Horima


Kenaka anthu a fuko la Yuda anapita pamodzi ndi abale awo a fuko la Simeoni ndi kukagonjetsa Akanaani amene amakhala ku Zefati, ndipo mzindawo anawuwononga kwambiri. Choncho mzindawo anawutcha Horima.


a ku Horima, Borasani, Ataki,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa