Numeri 2:18 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Kumadzulo kudzakhala magulu a msasa wa Efereimu pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Aefereimuwo ndi Elisama mwana wa Amihudi. Onani mutuwoBuku Lopatulika18 Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 “Mbali yakuzambwe kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Efuremu, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Efuremulo ndi Elisama mwana wa Amihudi, Onani mutuwo |
Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa; nyanga zake zili ngati za njati. Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina, ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu; nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”