Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 2:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Owerengedwa onse a chigono cha Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi chimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Owerengedwa onse a chigono cha Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi chimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Rubeni, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 151,450. Iwo akhale a gulu lachiŵiri poyenda.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 2:16
5 Mawu Ofanana  

Kenaka magulu a msasa wa fuko la Rubeni ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Elizuri mwana wa Sedeuri.


Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650.


Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka.


Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo.


Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa