Numeri 19:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Zitatha izi, wansembeyo ayenera kuchapa zovala zake ndiponso asambe ndi madzi. Iye angathe kupita ku msasa, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Onani mutuwoBuku Lopatulika7 Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Tsono wansembe achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, pambuyo pake aloŵe m'mahema. Koma wansembeyo adzakhale woipitsidwa mpaka madzulo. Onani mutuwo |
Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa.