Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 19:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Eliezara wansembe atengeko ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake ndi kuwaza kasanu nʼkawiri ku tsogolo kwa tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wake ndi chala chake, nawazeko mwazi wake kasanu ndi kawiri pakhomo pa chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wake ndi chala chake, nawazeko mwazi wake kasanu ndi kawiri pakhomo pa chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono wansembe Eleazara atengeko magazi a ng'ombeyo ndi chala chake, ndipo awaze magaziwo kumaso kwa chihema chamsonkhano kasanunkaŵiri.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 19:4
7 Mawu Ofanana  

Ndipo atenge magazi ena a ngʼombeyo, awawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha kummawa; kenaka awaze magaziwo ndi chala chake kasanu ndi kawiri patsogolo pa chivundikirocho.


Magazi ena awawaze pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kawiri kuliyeretsa ndi kulipatula kuchotsa zodetsa za Aisraeli.


Aviyike chala chake mʼmagaziwo ndi kuwawaza pamaso pa Yehova kasanu ndi kawiri patsogolo pa nsalu yotchinga.


Iye aviyike chala chake mʼmagazi, ndipo awawaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani yotchinga malo wopatulika.


Kwa Yesu mʼkhalapakati wa pangano latsopano, ndiponso mwafika ku magazi owazidwa amene amayankhula mawu abwino kuposa magazi a Abele.


Mulungu Atate anakusankhani, atakudziwani kuyambira pachiyambi, ndipo Mzimu Woyera wakuyeretsani kuti mumvere Yesu Khristu ndikutsukidwa ndi magazi ake. Chisomo ndi mtendere zikhale ndi inu mochuluka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa