Numeri 18:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 “Inuyo muzisamalira malo wopatulika ndi guwa lansembe, kuti ukali wa Yehova usawagwerenso Aisraeli. Onani mutuwoBuku Lopatulika5 Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Mudzatumikira pa ntchito za m'malo opatulika ndi pa ntchito za guwa, kuti mkwiyo usaŵagwerenso Aisraele. Onani mutuwo |
Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto.