Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 17:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkulu yense wa nyumba za makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkulu yense wa nyumba za makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi. Pakuti payenera kukhala ndodo imodzi pa mtsogoleri aliyense wa fuko la makolo ake.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 17:3
10 Mawu Ofanana  

Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137.


Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137.


kuti munalakwitsa kwambiri. Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu nʼkumati ‘Mukatipempherere kwa Yehova Mulungu wathu, nʼkudzatiwuza chimene afuna kuti tichite, ndipo ife tidzachita.’


“Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisraeli oyanjana nawo.’ Utengenso ndodo ina ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Efereimu, ndiye kuti fuko la Yosefe ndi Aisraeli onse oyanjana nawo.’


“Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake.


Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe.


Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu.


Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.


Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa