Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 17:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Ulankhule ndi Aisraele kuti akupatse ndodo, fuko lililonse ndodo imodzi. Atsogoleri ao onse akupatse ndodo khumi ndi ziŵiri molingana ndi mafuko a makolo ao. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 17:2
18 Mawu Ofanana  

Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda, udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse, mpaka mwini wake weniweni atabwera ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.


Ndipo anazigawa kwa ansembe amene analembetsa mayina awo mwa mbiri ya mabanja awo, chimodzimodzinso Alevi amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira molingana ndi udindo wawo ndi magulu awo.


Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni; udzalamulira pakati pa adani ako.


Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa.


Tsono uwagwiritse ntchito podzoza tenti ya msonkhano, Bokosi la Chipangano,


Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.”


Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.”


Moto unatulukanso mu mtengomo ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake. Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo yoyenera kupangira ndodo yaufumu. Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ ”


Lanoledwa kuti likaphe, lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi! “ ‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo.


“ ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’


Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza, nkhosa zimene ndi cholowa chanu, zimene zili zokha mʼnkhalango, mʼdziko la chonde. Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi monga masiku akale.


Yehova anawuza Mose kuti,


Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse.


Mose atamaliza kuyimika chihema chija, anachidzoza mafuta ndi kuchipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa