Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 17:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Apo Chauta adauza Mose kuti, “Kabwezere ndodo ya Aroni patsogolo pa bokosi laumboni. Uisunge kuti ikhale chenjezo kwa anthu oukira aja, kuti aleke kuŵiringulako, kuti angafe.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 17:10
23 Mawu Ofanana  

Ine ndili pakati pa mikango, ndagona pakati pa zirombo zolusa; anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi, malilime awo ndi malupanga akuthwa.


Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”


Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aaroni anayika mtsuko uja pafupi ndi bokosi la Chipangano kuti manawo asungike.


Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi! Pakuti Yehova wanena kuti, “Ndinabala ana ndi kuwalera, koma anawo andiwukira Ine.


“Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya, ndipo wakhala uli pomwepo. Kodi nkhondo sinagonjetse anthu ochita zoyipa ku Gibeya?


Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa pansi chafufumimba pamaso pa Aisraeli onse omwe anasonkhana pamenepo.


“Chokani pakati pa gulu ili kuti ndithetse mkanganowu kamodzinʼkamodzi.”


Izi ndi zofukizira za anthu omwe anafa chifukwa cha uchimo wawo. Musule zofukizirazo kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, chifukwa zinaperekedwa kwa Yehova ndipo ndi zopatulika. Zimenezi zikhale chizindikiro kwa Aisraeli.”


monga momwe Yehova anamulangizira kudzera mwa Mose. Chimenechi chinali chikumbutso kwa Aisraeli kuti munthu wina aliyense, kupatula zidzukulu za Aaroni, sayenera kupsereza lubani pamaso pa Yehova, kuopa kuti munthu woteroyo angakhale ngati Kora ndi omutsatira ake.


Mose anachita monga Yehova anamulamulira.


Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe.


Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake.


Choncho Mose anatenga ndodo pamaso pa Yehova monga momwe anamulamulira.


“Onetsetsani kuti mabanja a fuko la Kohati asachotsedwe kwa Alevi.


Ndipo osamawiringula, monga ena mwa iwo anachitira naphedwa ndi mngelo wowononga.


Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera.


Kuyambira pamene ndinakudziwani, mwakhala owukira Yehova.


Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova.


Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano.


Ana a Eli anali ana achabechabe pakuti samasamala za Yehova.


Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa