Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 16:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Kora mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Perezi, ana a Rubeni, anayamba kudzikuza,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Kora mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, ndiponso Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Peleti, adzukulu a Rubeni,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 16:1
11 Mawu Ofanana  

Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni, amene Yehova anadzipatulira.


Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137.


Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.


Ana a Izihari anali Kora, Nefegi ndi Zikiri.


Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”


“Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna.


ndi zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu mwana wa Rubeni, pamene nthaka inatsekula pakamwa pake pakati pa Aisraeli onse ndi kuwameza pamodzi ndi katundu wawo, matenti awo ndi chilichonse chawo.


Tsoka kwa iwo chifukwa anatsatira njira ya Kaini. Iwo athamangira phindu, nʼchifukwa chake anagwa mʼtchimo la Baalamu. Iwo anawonongedwa chifukwa chowukira monga anachitira Kora.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa