Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 15:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “ ‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pamene mupereka ng'ombe yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yopsereza kapena nsembe yopembedzera, kapena kuti zichitikedi zimene mudalumbira, kapena kuti ikhale nsembe yachiyanjano,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 15:8
10 Mawu Ofanana  

“ ‘Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya ngʼombe, ikhale yayimuna yopanda chilema. Aziyipereka pa khomo la tenti ya msonkhano, kuti Yehova alandire.


Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe awotche nyama yonse paguwapo. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chowotcha pa moto, cha fungo lokomera Yehova.


Pamene wina aliyense abweretsa ngʼombe kapena nkhosa kuti ikhale nsembe yachiyanjano kwa Yehova, kukwaniritsa zimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, nyamayo iyenera kukhala yangwiro ndi yopanda chilema kuti ilandiridwe.


“ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, ndipo choperekacho nʼkukhala ngʼombe yayimuna kapena yayikazi, ikhale yopanda chilema.


Ndipo ana a Aaroni atenthe zimenezi pa guwa, pamwamba pa chopereka chopsereza chimene chili pa nkhuni zoyakazo. Imeneyi ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Yehova.


ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa.


ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova.


pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri.


Atenge ngʼombe yayimuna yayingʼono ndi chopereka cha chakudya cha ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Atengenso ngʼombe ina yayimuna, yayingʼono, ya chopereka chopepesera machimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa