Numeri 15:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi. Onani mutuwoBuku Lopatulika4 pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Tsono amene adzabwere ndi zoperekayo, adzapereke kwa Chauta chopereka cha chakudya, cholemera kilogaramu limodzi, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi. Onani mutuwo |
Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo.