Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 14:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 koma musawukire Yehova. Komanso musaope anthu a mʼdzikomo, pakuti tidzawagonjetsa. Chitetezo chawachokera, koma ife Yehova ali nafe. Musawaope.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma musagalukire Chauta. Musaope anthu a m'dzikolo chifukwa tidzaŵaononga. Iwowo alibe oŵatchinjiriza, koma ife Chauta ali nafe, musaŵaope.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:9
50 Mawu Ofanana  

Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu.


Mulungu ali nafe pakuti ndiye mtsogoleri wathu. Ansembe ake atanyamula malipenga, adzayimba mfuwu wankhondo kulimbana nanu. Inu Aisraeli musalimbane ndi Yehova, Mulungu wa makolo anu, pakuti simungathe kupambana.”


Iye anapita kukakumana ndi Asa ndipo anati kwa iye, “Tandimverani, inu Asa ndi Ayuda onse ndi Benjamini. Yehova ali ndi inu, inunso mukakhala naye. Ngati inu mumufunafuna Iye mudzamupeza, koma ngati mumusiya, Iye adzakusiyani.


Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”


Iye ali ndi mphamvu ya anthu basi, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kutithandiza ndi kuchita nkhondo zathu.” Ndipo anthu anapeza chilimbikitso kuchokera pa zimene Hezekiya mfumu ya Yuda ananena.


Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.”


Motero iwo ananyoza dziko lokoma; sanakhulupirire malonjezo ake.


Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.


Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse? Akudya anthu anga ngati chakudya chawo ndipo satamanda Yehova?


Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.


Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.


Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova, chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.


Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.


Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.


Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso.


Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?”


Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi! Pakuti Yehova wanena kuti, “Ndinabala ana ndi kuwalera, koma anawo andiwukira Ine.


Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe, adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu, ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.


Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.


Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi, iwe wochepa mphamvu Israeli, chifukwa Ine ndidzakuthandiza,” akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.


Komabe iwo anawukira ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera. Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo ndipo Iye mwini anamenyana nawo.


Iwo adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, popeza Ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.


Musayiope mfumu ya ku Babuloni, imene mukuyiopa tsopano. Musachite nayo mantha, akutero Yehova, pakuti Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani ndi kukulanditsani mʼmanja mwake.


“Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni chifukwa chotopa. Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni, malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni. Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu, dziko la anthu onyada.


tachimwa ndipo tachita zolakwa ndi zoyipa. Takuwukirani posiya malangizo ndi malamulo anu.


Ambuye Mulungu wathu ndi wachifundo ndi wokhululuka, ngakhale kuti tamuwukira:


Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.”


Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo.


Kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa, choncho anthuwo anasonkhana motsutsana ndi Mose ndi Aaroni.


“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto ali ndi mphamvu ngati za njati. Amawononga mitundu yomuwukira ndi kuphwanya mafupa awo, amalasa ndi mivi yake.


“Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”


Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani?


Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi.”


Koma inu simunafune kupitako ndipo munawukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.


Ndipo ine ndinati kwa inu, “Musachite mantha kapena kuwaopa.


Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”


Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima.”


Mivi yanga idzakhuta magazi awo pamene lupanga langa lidzawononga mnofu: magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa ukapolo, mitu ya atsogoleri a adani.’ ”


Koma musachite nawo mantha, kumbukirani bwino zimene Yehova Mulungu wanu anachita ndi Farao pamodzi ndi Igupto yense.


Musaopsedwe nawo pakuti Yehova Mulungu wanu, amene ali pakati panu, ndi Mulungu wamkulu ndi woopsa.


Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova.


Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino


Palibe munthu amene adzatha kukugonjetsa masiku onse a moyo wako. Monga Ine ndinakhalira ndi Mose, chomwechonso ndidzakhala nawe. Sindidzakusiya kapena kukataya.


Tsopano ndipatseni dziko la ku mapiri limene Yehova anandilonjeza tsiku lija. Inu munamva nthawi ija kuti Aanaki anali kumeneko ndipo kuti mizinda yawo inali ikuluikulu ndi yotetezedwa. Komabe Yehova atakhala nane ndidzawathamangitsa monga Iye ananenera.”


A banja la Yosefe nawonso anathira nkhondo mzinda wa Beteli, ndipo Yehova anali nawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa