Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 14:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno!

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Aisraele onse adayamba kuŵiringulira Mose ndi Aroni. Mpingo wonse udaŵauza kuti, “Kukadakhala bwino tikadangofera ku Ejipito, kapena m'chipululu mommuno.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:2
31 Mawu Ofanana  

ndipo Eliyayo anayenda ulendo wa tsiku limodzi mʼchipululu. Anafika pa kamtengo ka tsache, nakhala pansi pa tsinde lake napemphera kuti afe. Iye anati, “Yehova, ine ndatopa nazo. Chotsani moyo wanga. Ineyo sindine wopambana makolo anga.”


“Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba?


Motero iwo ananyoza dziko lokoma; sanakhulupirire malonjezo ake.


Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo ndipo sanamvere Yehova.


Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.


Iwo anafunsa Mose kuti, “Kodi nʼchifukwa chakuti kunalibe manda ku dziko la Igupto kuti iwe utibweretse muno mʼchipululu kuti tidzafe? Chimene watichitachi nʼchiyani, kutitulutsa mʼdziko la Igupto?


Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”


Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?”


Ndipo tsopano, Inu Yehova, ingondiphani basi, pakuti ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”


Dzuwa litatuluka, Yehova anabweretsa mphepo yotentha yochokera kummawa, ndipo dzuwa linatentha pamutu pa Yona kotero analenguka nalo. Iye anangofuna atafa, ndipo anati, “Ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”


Anthu atadandaula kwa Yehova chifukwa cha mavuto awo, Yehovayo anamva ndipo anakwiya kwambiri. Kenaka moto wa Yehova unayaka pakati pawo ndi kutentha zigawo zina za kunja kwa msasa.


Ngati umu ndi mmene muzichitira nane, chonde ingondiphani pompano. Koma ngati mwandikomera mtima ndiye ndisaonenso mavutowa.”


Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo.


Usiku umenewo gulu lonse la Aisraeli linalira mofuwula kwambiri.


palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinazichita ku Igupto ndi mʼchipululu muno, koma osandimvera ndi kundiyesa kokwanira kakhumi,


Kodi sikukwanira kuti unatitulutsa, kutichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphe mʼchipululu muno? Kodi tsopano ukufunanso kutilemetsa?


Tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisraeli linatsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Iwo anati, “Inu mwapha anthu a Yehova.”


Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo.


Kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa, choncho anthuwo anasonkhana motsutsana ndi Mose ndi Aaroni.


Anakangana ndi Mose kuti, “Kunali bwino ifenso tikanangofa pamene abale athu anafa pamaso pa Yehova!


Chifukwa chiyani unabweretsa gulu la Yehova mʼchipululu muno, kuti ife ndi ziweto zathu tife kuno?


ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.”


Ndipo osamawiringula, monga ena mwa iwo anachitira naphedwa ndi mngelo wowononga.


Inu munanyinyirika mʼmatenti anu nʼkumati, “Mulungu amatida nʼchifukwa chake anatitulutsa ku Igupto kuti atipereke mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge.


Ndipo Yehova atakutulutsani ku Kadesi Barinea anati, “Pitani mukatenge dziko limene ndakupatsani.” Koma munawukira ulamuliro wa Yehova Mulungu wanu. Inu simunamukhulupirire kapena kumumvera.


Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto?


Anthu amenewa amangʼungʼudza ndi kudandaula. Amatsatira zilakolako zawo zoyipa. Amayankhula zodzitamandira ndipo amanamiza ena pofuna kupeza phindu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa